Joshua 5:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina pamene Yoswa anali pafupi ndi Yeriko, mwadzidzidzi adaona munthu ataimirira kutsogolo kwake, lupanga losolola lili m'manja. Tsono Yoswa adapita pomwe panali munthupo, namufunsa kuti, “Kodi iwe ndiwe mmodzi wa ankhondo athu kapena ndiwe mdani wathu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pokhala Yoswa ku Yeriko, anakweza maso ake, napenya, ndipo taona, panaima munthu pandunji pake ndi lupanga lake losolola m'dzanja lake; namuka Yoswa kuli iye, nati iye, Uvomerezana ndi ife kapena ndi adani athu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina pamene Yoswa anali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo mwadzidzidzi anaona munthu atayima patsogolo pake ndi lupanga losolola mʼdzanja lake. Yoswa anapita pamene panali munthuyo ndipo anamufunsa kuti, “Kodi uli mbali yathu kapena ya adani athu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pokhala Yoswa ku Yeriko, anakweza maso ace, napenya, ndipo taona, panaima muthu pandunji pace ndi lupanga lace losolola m'dzanja lace; namuka Yoswa kuli iye, nati iye, Ubvomerezana ndi ife kapena ndi aelani athu?