Joshua 5:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu uja adayankha kuti, “Sindine mmodzi mwa ankhondo anu kapenanso mdani wanu. Ndine mtsogoleri wa gulu lankhondo la Chauta pano.” Choncho Yoswa adadzigwetsa pansi chafufumimba naati, “Ine ndine wantchito wanu, mbuyanga. Nanga mufuna kuti ndichite chiyani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati, Iai, koma ndadza ine, kazembe wa ankhondo a Yehova. Pamenepo Yoswa anagwa nkhope yake pansi, napembedza, nati kwa iye, Anenanji Ambuyanga kwa mtumiki wake?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti “Sindili mbali iliyonse. Ndabwera monga mkulu wa asilikali a Yehova.” Pomwepo Yoswa anadzigwetsa chafufumimba kupereka ulemu, ndipo anamufunsa, “Kodi mbuye wanga muli ndi uthenga wotani kwa mtumiki wanu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati, lai, koma ndadza ine, kazembe wa ankhondo a Yehova. Pamenepo Yoswa anagwa nkhope yace pansi, napembedza, nati kwa iye, Anenanji Ambuyanga kwa mtumiki wace?