Joshua 5:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wolamula gulu lankhondo la Chauta uja adamuyankha kuti, “Vula nsapato zako. Malo amene ukuimirirapoŵa ngoyera.” Yoswa adachitadi zimene adamuuzazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kazembe wa ankhondo a Yehova anati kwa Yoswa, Vula nsapato yako pa phazi lako; pakuti malo upondapo mpopatulika. Nachita Yoswa chomwecho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkulu wa asilikali a Yehova uja anayankha kuti, “Vula nsapato zako, pakuti wayima pa malo wopatulika.” Ndipo Yoswa anachitadi zimene anawuzidwazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kazembe wa ankhondo a Yehova anati kwa Yoswa, Bvula nsapato yako pa phazi lako; pakuti malo upondapo mpopatulika. Nacita Yoswa comweco.