Joshua 5:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adachita zimenezi chifukwa amuna amene anali oyenera kuponya nkhondo onse adaatha nkufa m'chipululu atatuluka ku Ejipito kuja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma chifukwa chakuti Yoswa anawadula ndi ichi: anthu onse otuluka m'Ejipito, anthu amuna, ndiwo amuna onse ankhondo, adafa m'chipululu panjira, atatuluka m'Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chimene Yoswa anachitira izi ndi ichi: Onse amene anatuluka mʼdziko la Igupto, amuna onse amene anali oyenera kumenya nkhondo anatha kufa mʼchipululu atatuluka mʼdziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma cifukwa cakuti Yoswa anawadula ndi ici: anthu onse oturuka m'Aigupto, anthu amuna, ndiwo amuna onse ankhondo, adafa m'cipululu panjira, ataturuka m'Aigupto.