Joshua 5:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele adakhala akuyenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka adafa amuna onse amene potuluka ku Ejipito anali a msinkhu woyenera pa nkhondo. Adatha nkufa, popeza kuti sadamvere Chauta. Iye adaachita kuŵalumbirira kuti sadzaloŵamo m'dziko lamwanaalirenji lija limene adaalonjeza kwa makolo ao kuti adzaŵapatsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka m'Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anakhala akuyenda mʼchipululu kwa zaka makumi anayi mpaka amuna onse amene potuluka mʼdziko la Igupto anali a msinkhu woyenera kupita ku nkhondo anamwalira. Iwo anafa chifukwa sanamvere mawu a Yehova. Yehova anawalumbirira kuti sadzalowa konse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi limene analonjeza kwa makolo awo kuti adzatipatsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ana a Israyeli anayenda m'cipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo oturuka m'Aigupto udatha, cifukwa ca kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci.