Joshua 5:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adauza Yoswa kuti, “Lero ndakuchotserani manyazi a ukapolo wanu uja umene munali nawo ku Ejipito.” Nchifukwa chake malowo adaŵatcha Giligala, ndipo mpaka lero lino malo ameneŵa akudziŵika ndi dzina limeneli.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndakukunkhunizirani mtonzo wa Ejipito. Chifukwa chake dzina la malowo analitcha Giligala kufikira lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Kuyambira tsopano anthu a ku Igupto sadzakunyozaninso.” Nʼchifukwa chake malowa anatchedwa Giligala mpaka lero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero Uno ndakukunkhunizirani mtonzo wa Aigupto, Cifukwa cace dzina la malowo analicha Giligala kufikira lero lino.