Joshua 6:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzinda wa Yeriko udaali utatsekedwa pa zipata zake zonse, kuti Aisraele asaloŵe. Panalibe ndi mmodzi yemwe wotuluka kapena kuloŵa mumzindamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ku Yeriko anatseka pazipata, natsekedwa chifukwa cha ana a Israele, panalibe wotuluka, panalibenso wolowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mzinda wa Yeriko unali utatsekedwa kuti Aisraeli asalowe. Palibe amene amatuluka kapena kulowa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ku Yeriko anatseka pazipata, natsekedwa cifukwa ca ana a Israyeli, panalibe woturuka, panalibenso wolowa.