Joshua 6:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yoswa adalamula anthu kuti asafuule kapena kuchita phokoso mpaka iye atalamula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa analamulira anthu, ndi kuti, Musamafuula, kapena kumveketsa mau anu, asatuluke konse mau m'kamwa mwanu, mpaka tsiku lakunena nanu ine, Fuulani; pamenepo muzifuula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yoswa nʼkuti atalamulira anthu kuti, “Musafuwule, musakweze mawu anu kapena kuyankhula mpaka tsiku limene ndidzakuwuzani kuti mufuwule. Pamenepo mudzafuwule!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa analamulira anthu, ndi kuti, Musamapfuula, kapena kumveketsa mau anu, asaturuke konse mau m'kamwa mwanu, mpaka tsiku lakunena nanu ine, Pfuulani; pamenepo muzipfuula.