Joshua 6:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, adadzuka m'mbandakucha, ndipo adazungulira mzindawo kasanunkaŵiri. Ndi pa tsiku limenelo lokha pomwe adazungulira mzindawo kasanunkaŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri analawira mamawa, mbandakucha, nazungulira mudzi mommuja kasanu ndi kawiri; koma tsiku lijalo anazungulira mudzi kasanu ndi kawiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, anadzuka mʼbandakucha ndipo anazungulira mzindawo kasanu ndi kawiri. Ndi pa tsiku lokhali limene anazungulira mzindawu kasanu ndi kawiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, tsiku lacisanu ndi ciwiri analawira mamawa, mbandakuca, nazungulira mudzi mommuja kasanu ndi kawiri; koma tsiku lijalo anazungulira mudzi kasanu ndi kawiri.