Joshua 6:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuzungulira kwakasanunkaŵiri kutatha, ansembe aja akuliza malipenga, Yoswa adauza anthu kuti, “Fuulani! Chauta wakupatsani mzindawu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pa nthawi yachisanu ndi chiwiri, pamene ansembe analiza mphalasa, Yoswa anati kwa anthu, Fuulani; pakuti Yehova wakupatsani mudziwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pomwe amazungulira kachisanu ndi chiwiri, ansembe akuliza malipenga mokweza, Yoswa analamulira anthu kuti “Fuwulani pakuti Yehova wakupatsani mzindawu!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pa nthawi yacisanu ndi ciwiri, pamene ansembe analiza mphalasa, Yoswa anati kwa anthu, Pfuulani; pakuti Yehova wakupatsani mudziwo.