Joshua 6:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzindawu pamodzi ndi zonse za m'menemu muwononge, kuti zikhale ngati nsembe zopereka kwa Chauta. Koma Rahabu yekha wadama uja ndi onse a m'nyumba mwake, muŵasunge poti ndiye adabisa azondi athu aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mudziwo udzaperekedwa kwa Yehova ndi kuonongeka konse, uwu ndi zonse zili m'mwemo; Rahabi yekha wadamayo adzakhala ndi moyo, iye ndi onse ali naye m'nyumba, chifukwa anabisa mithenga tinawatumawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mzindawu ndi zonse zimene zili mʼmenemo muziwononge. Rahabe yekha, mayi wadama, ndi aliyense amene ali pamodzi naye mʼnyumba mwake asaphedwe, chifukwa anabisa anthu odzazonda, amene ife tinawatuma
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mudziwo udzaperekedwa kwa Yehova ndi kuonongeka konse, uwu ndi zonse ziri m'mwemo; Rahabi yekha wadamayo adzakhala ndi moyo, iye ndi onse ali naye m'nyumba, cifukwa anabisa mithenga tinawatumawo.