Joshua 6:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo ansembe adalizanso malipenga aja. Anthu atamva, adafuula kwambiri, ndipo linga la mzindawo lidagwa. Ndipo ankhondo onse adabwera nakaloŵa mu mzindawo, naulanda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anafuula, naliza mphalasa ansembe; ndipo kunali, pamene anthu anamva kulira kwa mphalasa, anafuula anthu ndi mfuu yaikulu, niligwa linga pomwepo; nakwera anthu kulowa m'mudzi, yense kumaso kwake; nalanda mudziwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ansembe analiza malipenga. Anthu atamva kulira kwa malipenga, anafuwula kwambiri ndipo makoma a Yeriko anagwa. Choncho ankhondo anabwera ku mzinda uja nawulanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anapfuula, naliza mphalasa ansembe; ndipo kunali, pamene anthu anamva kulira kwa mphalasa, anapfuula anthu ndi mpfuu yaikuru, niligwa linga pomwepo; nakwera anthu kulowa m'mudzi, yense kumaso kwace; nalanda mudziwo.