Joshua 6:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adaloŵa mu mzinda, malupanga ali m'manja, napha onse ndi lupanga, kuyambira amuna, akazi, ana ndi nkhalamba zomwe. Adaphanso zoŵeta zonse, monga ng'ombe, nkhosa ndi abulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapereka kuziononga ndi lupanga lakuthwa zonse za m'mudzi, amuna ndi akazi omwe, ana ndi nkhalamba zomwe, kudza ng'ombe, ndi nkhosa, ndi abulu, ndi lupanga lakuthwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo analowa mu mzindawo nawononga ndi lupanga chilichonse chamoyo kuyambira amuna, akazi, ana ndi akulu, ngʼombe, nkhosa ndi abulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapereka kuziononga ndi lupanga lakuthwa zonse za m'mudzi, amuna ndi akazi omwe, ana ndi nkhalamba zomwe, kudza ng'ombe, ndi nkhosa, ndi aburu, ndi lupanga lakuthwa.