Joshua 6:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yoswa adauza anthu aŵiri amene adakazonda aja kuti, “Pitani ku nyumba ya mkazi wadamayo, ndipo iye pamodzi ndi onse a m'nyumba mwake abwere kuno, monga mudamlonjezera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa ananena kwa amuna awiri anazonda dzikowo, Lowani m'nyumba ya mkazi wadamayo, ndi kutulutsamo mkaziyo ndi zonse ali nazo, monga munamlumbirira iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoswa anawuza anthu awiri amene anakazonda dziko aja kuti, “Pitani ku nyumba ya mkazi wadama uja ndipo mukamutulutse iye pamodzi ndi onse amene ali naye ndipo mukabwere nawo kuno, munamulumbirira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa ananena kwa amuna awiri anazonda dzikowo, Lowani m'nyumba ya mkazi wadamayo, ndi kuturutsamo mkaziyo ndi zonse ali nazo, monga munamlumbirira iye.