Joshua 6:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yoswa adamsiya ali moyo Rahabu wadama uja, pamodzi ndi abale ake onse, poti ndiye adaabisa azondi aja amene Yoswayo adaaŵatuma kukazonda Yeriko. Zidzukulu zake za Rahabu zilipo pakati pa Aisraele mpaka lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Rahabi, mkazi wadamayo ndi banja la atate wake, ndi onse anali nao, Yoswa anawasunga ndi moyo; ndipo anakhala pakati pa Israele mpaka lero lino; chifukwa anabisa mithenga imene Yoswa anaituma kuzonda Yeriko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yoswa sanaphe Rahabe, mkazi wadamayo pamodzi ndi banja lake ndi onse amene anali naye, chifukwa anabisa anthu amene iye anawatuma kukazonda Yeriko. Zidzukulu zake za Rahabeyo zikukhala pakati pa Aisraeli mpaka lero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Rahabi, mkazi wadamayo ndi banja la atate wace, ndi onse anali nao, Yoswa anawasunga ndi moyo; ndipo anakhala pakati pa Israyeli mpaka lero tino; cifukwa anabisa mithenga imene Yoswa anaituma kuzonda Yeriko.