Joshua 6:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi imeneyo Yoswa adapereka chenjezo motemberera kuti, “Aliyense amene adzamangenso mzinda wa Yerikowu, Chauta adzamtemberere. Aliyense amene adzamange maziko ake, mwana wake wachisamba adzafa. Aliyense amene adzamange zipata zake, mzime wake adzafa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mudzi uwu wa Yeriko; adzamanga kuzika kwake ndi kutayapo mwana wake woyamba, nadzaimika zitseko zake ndi kutayapo mwana wake wotsirizira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi imeneyo Yoswa anapereka chenjezo motemberera kuti, “Akhale wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzamangenso mzinda uwu wa Yeriko: “Aliyense amene adzayike maziko ake, mwana wake wamwamuna wachisamba adzafa, aliyense womanga zipata zake mwana wake wamngʼono adzafa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mudzi uwu wa Yeriko; adzamanga kuzika kwace ndi kutayapo mwana wace woyamba, nadzaimika zitseko zace ndi kutayapo mwana wace wotsirizira.