Joshua 6:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adzalize mosalekeza ndi mwamphamvu zedi. Ndipo anthu akadzangomva kuliza koteroko, adzafuule kolimba, motero makoma a mzindawo adzagwa. Apo ankhondo ako onse adzaloŵa mumzindamo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzakhala kuti akaliza chilizire ndi nyanga ya nkhosa yamphongo, nimumva kulira kwa mphalasa, anthu onse afuule mfuu yaikulu; ndipo linga la mudziwo lidzagwa pomwepo, ndi anthu adzakwera ndi kulowamo yense kumaso kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ansembe adzalize malipenga kosalekeza. Tsono anthu onse akadzamva kuliza kumeneku adzafuwule kwambiri, ndipo makoma a mzindawo adzagwa. Zikadzatero ankhondo adzalowe mu mzindawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzakhala kuti akaliza cilizire ndi nyanga ya nkhosa yamphongo, nimumva kulira kwa mphalasa, anthu onse apfuule mpfuu yaikuru; ndipo linga la mudziwo lidzagwa pomwepo, ndi anthu adzakwera ndi kulowamo yense kumaso kwace.