Joshua 7:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Aisraele ena sadamvere lamulo la Chauta loti asatenge kanthu kena kalikonse koyenera kuwonongedwa. Tsono amene adaagwinyako zinthuzo, anali Akani. Iyeyu anali mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda. Choncho Chauta adakwiyira Aisraele onse kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ana a Israele analakwa ndi choperekedwacho; popeza Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anatapa choperekedwacho; ndi mkwiyo wa Yehova unayakira ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Aisraeli anachita zachinyengo ndi lamulo lija loti asatenge kalikonse koyenera kuwonongedwa. Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda anatengako zinthu zina. Choncho Yehova anakwiyira Israeli kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ana a Israyeli analakwa ndi coperekedwaco; popeza Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa pfuko la Yuda, anatapa coperekedwaco; ndi mkwiyo wa Yehova unayakira ana a Israyeli.