Joshua 7:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele ena adachimwa. Chipangano chija ndidapangana nawochi sadasunge. Zinthu zija ndidaŵauza kuti aonongezi, adagwinyako. Adabako, ndi kunenanso bodza, namaika zinthu zakubazo pakati pa zinthu zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Israele wachimwa, nalakwiranso chipangano changa, ndinawalamuliracho; natengakonso choperekedwacho; anabanso, nanyenganso, nachiika pakati pa akatundu ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli achimwa. Iwo aphwanya pangano limene ndinawalamula kuti asunge. Anatengako zinthu zina zofunika kuwonongedwa. Choncho anabako, ananena bodza ndi kuyika zinthu zakubazo pamodzi ndi katundu wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Israyeli wacimwa, nalakwiranso cipangano canga, ndinawalamuliraco; natengakonso coperekedwaco; anabanso, nanyenganso, naciika pakati pa akatundu ao.