Joshua 7:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Aisraele sangathe kulimbana ndi adani ao. Athaŵa pamaso pa adani ao chifukwa choti iwowo ngoyenera kuwonongedwa. Sindidzakhala nawonso mpaka utaononga zinthu zimene ndidakulamula kuti usatenge.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa ichi ana a Israele sangathe kuima pamaso pa adani ao, awafulatira adani ao, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga choperekedwacho, kuchichotsa pakati pa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Aisraeli sangathe kulimbana ndi adani awo. Iwo anathawa pamaso pa adani awo chifukwa ndiwo oyenera kuwonongedwa. Ine sindikhalanso ndi inu pokhapokha mutawononga chilichonse choyenera kuwonongedwa pakati panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa ici ana a Israyeli sangathe kuima pamaso pa adani ao, awafulatira adani ao, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga coperekedwaco, kucicotsa pakati pa inu.