Joshua 7:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyamuka, ukalamule anthu kuti adzipatule, kuti akonzekere kuwonana ndi Ine maŵa, chifukwa Ine Mulungu wa Aisraele ndidzaŵauza kuti, ‘Inu Aisraele, zinthu zija ndidaakuuzani kuti muwonongezi, zili pakati panu. Inu simungalimbe polimbana ndi adani anu, mpaka zinthu zimenezi mutachotsa.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tauka, patula anthu, nuti, Mudzipatulire mawa; pakuti atero Yehova Mulungu wa Israele, Pali choperekedwa chionongeke pakati pako, Israele iwe; sukhoza kuima pamaso pa adani ako, mpaka mutachotsa choperekedwacho pakati panu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nyamuka, ukawawuze anthu kuti, ‘Mudzipatule nokha kukonzekera kuonana nane mawa; pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti choyenera kuwonongedwa chija chili pakati panu, inu Aisraeli. Simungathe kulimbana ndi adani anu mpaka mutachichotsa.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tauka, patula anthu, nuti, Mudzipatulire mawa; pakuti atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Pali coperekedwa cionongeke pakati pako, Israyeli iwe; sukhoza kuima pamaso pa adani ako, mpaka mutacotsa coperekedwaco pakati panu.