Joshua 7:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero maŵa m'maŵa, mutulukire poyera nonsenu, fuko limodzilimodzi. Fuko limene Ine Chauta ndidzaliloze lidzabwera patsogolo, mbumba imodziimodzi. Mbumba imene ndidzailoze idzabwera patsogolo, banja limodzilimodzi. Banja limene ndidzaliloze lidzabwera patsogolo, munthu mmodzimmodzi
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma m'mawa adzakuyandikitsani, fuko ndi fuko; ndipo kudzali kuti fukoli Yehova aliwulula lidzayandikira mwa zibale zake; ndi chibale Yehova achiwulula chidzayandikira monga mwa a nyumba ake; ndi a m'nyumbawo Yehova awawulula adzayandikira mmodzimmodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mawa mmamawa adzabwere pamaso pa Yehova fuko limodzilimodzi. Fuko limene Yehova adzaliloze lidzabwere patsogolo mbumba imodziimodzi. Tsono mbumba imene Yehova adzayiloze idzabwere patsogolo banja limodzilimodzi. Banja limene Yehova adzaliloze lidzabwere patsogolo munthu mmodzimmodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma m'mawa adzakuyandikitsani, pfuko ndi pfuko; ndipo kudzali kuti pfukoli Yehova aliulula lidzayandikira mwa zibale zace; ndi cibale Yehova aciulula cidzayandikira monga mwa a nyumba ace; ndi a m'nyumbawo Yehova awaulula adzayandikira mmodzi mmodzi.