Joshua 7:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yemwe adzapezeke ndi zinthu zimenezo, adzatenthedwa pamodzi ndi banja lake lonse ndi zonse zomwe ali nazo. Chinthu chimene wachitacho nchoopsa, chifukwa waphwanya pangano lomwe anthu anga adachita ndi Ine.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzali kuti iye wogwidwa ali nacho choperekedwacho adzatenthedwa ndi moto, iye ndi zonse ali nazo chifukwa analakwira chipangano cha Yehova, ndi chifukwa anachita chopusa m'Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye amene adzagwidwe ndi zinthu zoyenera kuwonongedwazo adzawotchedwa ndi moto, pamodzi ndi banja lake lonse ndi zinthu zake zonse. Iyeyutu wachita chinthu chonyansa pakati pa Aisraeli ndi kuphwanya pangano limene anthu anga anachita ndi Ine!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzali kuti iye wogwidwa ali naco coperekedwaco adzatenthedwa ndi moto, iye ndi zonse ali nazo cifukwa analakwira cipangano ca Yehova, ndi cifukwa anacita copusa m'Israyeli.