Joshua 7:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbumba zonse za fuko la Yuda adazitulutsira poyera, ndipo mbumba ya Zera idagwidwa. Tsono mabanja a Zera adaŵatulutsira poyera, ndipo banja la Zabidi lidagwidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nayandikizitsa zibale za Yuda, nagwira chibale cha Azera; nayandikizitsa chibale cha Azera, mmodzimmodzi, nagwidwa Zabidi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anabweretsa poyera mbumba zonse za fuko la Yuda, ndipo mbumba ya Zera inagwidwa. Kenaka anatulutsa poyera mabanja onse a mbumba ya Zera ndipo banja la Zabidi linagwidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nayandikizitsa zibale za Yuda, nagwira cibale ca Azari; nayandikizitsa cibale ca Azari, mmodzi mmodzi, nagwidwa Zabidi;