Joshua 7:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pompo Yoswa adatulutsa anthu onse a banja la Zabidi, ndipo Akani adagwidwa. Iyeyo anali mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nayandikizitsa a m'nyumba yake mmodzimmodzi; ndipo Akani, mwana wa Karimi, mwanu wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda anagwidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Potsiriza anatulutsa anthu onse a banja la Zabidi ndipo Akani anagwidwa. Iyeyu anali mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera wa fuko la Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nayandikizitsa a m'nyumba yace mmodzi mmodzi; ndipo Akani, mwana wa Karimu, mwanu wa Zabidi, mwana wa Zera, wa pfuko la Yuda anagwidwa.