Joshua 7:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yoswa adauza Akani kuti, “Iwe mwana wanga, lemekeza Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndipo umtamande. Uze tsopano lino zimene wachita. Usati undibisire.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, uchitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israele, numlemekeze Iye; nundiuze tsopano, wachitanji? Usandibisire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yoswa anati kwa Akani, “Mwana wanga pereka ulemerero kwa Yehova Mulungu wa Israeli ndipo umuyamike Iye. Ndiwuze zimene wachita, ndipo usandibisire.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, ucitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israyeli, numlemekeze iye; nundiuze tsopano, wacitanji? usandibisire.