Joshua 7:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atagonjetsa Yeriko, Yoswa adatuma anthu ena kuti akazonde mzinda wa Ai. Mzinda umenewu unali kuvuma kwa Betele, pafupi ndi Betaveni. Ataŵatuma kuti akazonde mzindawo, anthu aja adapitadi nazonda mzinda wa Ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa anatuma amuna kuchokera ku Yeriko apite ku Ai, ndiwo pafupi pa Betaveni, kum'mawa kwa Betele; nanena nao, Kwerani ndi kukazonda dziko. Nakwera amunawo, nazonda Ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yoswa anatuma anthu kuchokera ku Yeriko kukazonda ku mzinda wa Ai umene uli pafupi ndi mzinda wa Beti-Aveni kummawa kwa Beteli, ndipo anawawuza kuti, “Pitani mukazonde chigawochi.” Anthuwo anapitadi kukazonda Ai.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa anatuma amuna kucokera ku Yeriko apite ku Ai, ndiwo pafupi pa Beti-aveni, kum'mawa kwa Beteli; nanena nao, Kwerani ndi kukazonda dziko. Nakwera amunawo, nazonda Ai.