Joshua 7:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pakati pa chuma chija, ndidaonapo mwinjiro wokongola wa ku Babiloni, ndi makilogramu aŵiri a siliva ndiponso munsi wa golide wolemera theka la kilogramu. Zonsezi ndidaazikhumba kwambiri, kotero kuti ndidatenga ndithu. Mungathe kuzipeza m'chithando changa m'mene ndidazibisa. Mukapezanso silivayo pansi pa zinthu zinazo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamene ndinaona pazofunkha malaya abwino a ku Babiloni, ndi masekeli mazana awiri a siliva, ndi chikute chagolide, kulemera kwake masekeli makumi asanu, ndinazikhumbira ndi kuzitenga; ndipo taonani, ndazibisa m'nthaka pakati pa hema wanga, ndi siliva pansi pakepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinaona mwa zinthu zolanda ku nkhondo zija, mkanjo wokongola wa ku Babuloni, makilogalamu awiri a siliva ndiponso golide wolemera theka la kilogalamu. Zimenezi ndinazikhumba ndipo ndinazitenga. Ndazibisa mʼkati mwa tenti yanga, ndipo siliva ali pansi pake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamene ndinaona pazofunkha maraya abwino a ku Babulo, ndi masekeli mazana awiri a siliva, ndi cikute cagolidi, kulemera kwace masekeli makumi asanu, ndinazikhumbira ndi kuzitenga; ndipo taonani, ndazibisa m'nthaka pakati pa hema wanga, ndi siliva pansi pacepo.