Joshua 7:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adazitulutsa zonsezo m'chithandomo, napita nazo kwa Yoswa ndi kwa Aisraele onse. Ndipo adaziika pamaso pa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anazichotsa pakati pa hema, nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa ana onse a Israele, nazitula pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anazichotsa zinthuzo mu tenti yake nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa Aisraeli onse ndipo anaziyika pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anazicotsa pakati pa hema, nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa ana onse a Israyeli, nazitula pamaso pa Yehova.