Joshua 7:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yoswa ndi Aisraele onse adamtenga Akani ndi zinthu zimene adapezeka nazo zija monga silivayo, mwinjiro ndi munsi wa golide uja. Adatenganso ana ake aamuna ndi aakazi omwe, ndi zoŵeta zake, ng'ombe, abulu, nkhosa, ndi hema lake ndi zonse zomwe anali nazo. Zonsezo adapita nazo ku chigwa chotchedwa Akori.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa, ndi Aisraele onse naye, anatenga Akani mwana wa Zera, ndi siliva, ndi malayawo, ndi chikute chagolide, ndi ana ake aamuna ndi aakazi, ndi ng'ombe zake, ndi abulu ake, ndi nkhosa zake, ndi hema wake ndi zake zonse; nakwera nazo ku chigwa cha Akori.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yoswa pamodzi ndi Aisraeli onse anatenga Akani mwana wa Zera pamodzi ndi siliva, mkanjo, golide zimene anapezeka nazo zija. Anatenganso ana ake aamuna ndi aakazi, ngʼombe zake, abulu ndi nkhosa, tenti yake ndi zonse anali nazo, kupita nazo ku chigwa cha Akori.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa, ndi Aisrayeli onse naye, anatenga Akani mwana wa Zera, ndi siliva, ndi marayawo, ndi cikute cagolidi, ndi ana ace amuna ndi akazi, ndi ng'ombe zace, ndi aburu ace, ndi nkhosa zace, ndi hema wace ndi zace zonse; nakwera nazo ku cigwa ca Akori.