Joshua 7:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yoswa adati, “Chifukwa chiyani watiputira mavuto otereŵa? Tsopano Chauta ndiye amene adzetse mavuto ameneŵa pa iwe!” Pompo anthu onsewo adamponya miyala Akani, namupha. Adaponya miyala banja lake lonse, mpakanso kulitentha pamodzi ndi zake zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa anati, Watisautsiranji? Yehova adzakusautsa lero lino. Ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nawatentha ndi moto, nawaponya miyala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoswa anati “Chifukwa chiyani wabweretsa mavuto awa pa ife? Yehova ndiye abweretse mavuto pa iwe lero.” Kenaka Aisraeli onse anaponya miyala Akani, namupha. Anaponyanso miyala banja lake lonse, nʼkulipha. Pambuyo pake anatentha Akani uja, banja lake ndi zonse zimene anali nazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa anati, Watisautsiranji? Yehova adzakusautsa lero lino. Ndipo, Aisrayeli onse anamponya miyala, nawatentha ndi moto, nawaponya miyala.