Joshua 7:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaunjika mulu waukulu wamiyala pa iyeyo, ndipo muluwo ulipo mpaka lero lino. Nchifukwa chake mpaka lero chigwa chimenechi amachitchula kuti “Chigwa cha Mavuto.” Motero mtima wa Chauta udatsika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuunjikira mulu waukulu wamiyala, wokhalako kufikira lero lino; ndipo Yehova anatembenuka kusiya mkwiyo wake waukulu. Chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Akori, mpaka lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawunjika mulu waukulu wa miyala pa Akani, imene ilipobe mpaka lero. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa chigwa cha Akori mpaka lero. Ndipo Yehova anachotsa mkwiyo wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuuniikira mulu waukuru wamiyala, wokhalako kufikira lero lino; ndipo Yehova anatembenuka kusiya mkwiyo wace waukuru. Cifukwa cace anacha dzina lace la malowo, Cigwa ca Akori, mpaka lero lino.