Joshua 7:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atabwerera kwa Yoswa, anthuwo adamuuza kuti, “Sikofunikira kuti tipite tonse kumeneko. Ingotumani anthu zikwi ziŵiri kapena zitatu kuti akathire nkhondo mzinda wa Ai. Musatume anthu onse kumeneko poti si mzinda waukulu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anabwera kwa Yoswa, nati kwa iye, Asakwere anthu onse; koma akwere amuna ngati zikwi ziwiri kapena zitatu kukantha Ai; musalemetsa anthu onse kumkako, pakuti a komweko ndi owerengeka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atabwera kwa Yoswa, anamuwuza kuti, “Sikofunika kuti apite anthu onse kukathira nkhondo mzinda wa Ai. Mutumizeko anthu 2,000 kapena 3,000 kuti akatenge mzindawo. Musawatume anthu onse kumeneko popeza kuli anthu ochepa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anabwera kwa Yoswa, nati kwa iye, Asakwere anthu onse; koma akwere amuna ngati zikwi ziwiri kapena zitatu kukantha Ai; musalemetsa anthu onse kumkako, pakuti a komweko ndi owerengeka;