Joshua 7:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Ai adathamangitsa Aisraele kuchokera ku chipata cha mzindawo mpaka ku ngwenya. Aisraele okwanira ngati 36 adaphedwa, makamaka pamene ankatsika phiri. Motero Aisraele onse adataya mtima, ndipo adachita mantha kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapirikitsa kuyambira pachipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Ai anathamangitsa Aisraeli kuchokera pa chipata cha mzindawo mpaka ku ngwenya ndipo anapha anthu 36. Iwowa anawapha pamene ankatsika phiri. Choncho mitima ya anthu inasweka ndipo analibenso mphamvu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapitikitsa kuyambira pacipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi.