Joshua 7:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akanani ndi anthu ena onse okhala m'dziko muno adzamva zimenezi, ndipo adzatizinga ndi kutipha tonse. Kodi pamenepa inu mudzachitapo chiyani kuti ulemu wanu usaonongeke?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akadzamva ichi Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu pa dziko lapansi; ndipo mudzachitiranji dzina lanu lalikulu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akanaani ndi anthu ena a dziko lino adzamva zimenezi ndipo adzatizinga ndi kutiwonongeratu. Nanga inu mudzatani ndi dzina lanu lamphamvulo?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akadzamva ici Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu pa dziko lapansi; ndipo mudzacitiranji dzina lanu lalikuru?