Joshua 8:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Chauta adauza Yoswa kuti, “Usachite mantha kapena kutaya mtima. Tenga ankhondo onse, ndipo upite nawo ku Ai. Ndidzapereka m'manja mwanu mfumu ya ku Ai pamodzi ndi anthu ake onse. Mzindawo pamodzi ndi dzikolo, zonsezo zidzakhala zanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Usaope, kapena kutenga nkhawa, tenga anthu onse a nkhondo apite nawe, ndipo tauka, kwera ku Ai; taona, ndapereka m'dzanja lako mfumu ya ku Ai, ndi anthu ake ndi mudzi wake ndi dziko lake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Usachite mantha kapena kutaya mtima. Tenga gulu lonse la nkhondo, ndipo upite ku Ai. Taona, ndapereka mfumu ya Ai pamodzi ndi anthu ake, mzinda wake ndi dziko lake lonse mʼmanja mwako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Usaope, kapena kutenga nkhawa, tenga anthu onse a nkhondo apite nawe, ndipo tauka, kwera ku Ai; taona, ndapereka m'dzanja lako mfumu ya ku Ai, ndi anthu ace ndi mudzi wace ndi dziko lace;