Joshua 8:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adakhazika ankhondo mokonzekera nkhondo, ndipo gulu lalikulu la ankhondowo lidamanga zithando cha kumpoto kwa mzinda, m'chigwamo, koma gulu lina lija lidakamanga chakuzambwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo anaika anthu, khamu lonse lokhala kumpoto kwa mudzi, ndi olalira ao kumadzulo kwa mudzi, ndipo usiku uja Yoswa analowa pakati pa chigwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anakhazika anthuwo mokonzekera nkhondo. Gulu lalikulu la nkhondo linakamanga zithando zawo kumpoto kwa mzinda, ndipo gulu lina linakamanga zithando zawo kumadzulo kwa mzindawo. Usiku umenewo Yoswa anakagona ku chigwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo anaika anthu, khamu lonse lokhala kumpoto kwa mudzi, ndi olalira ao kumadzulo kwa mudzi, ndipo usiku uja Yoswa analowa pakati pa cigwa,