Joshua 8:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ya ku Ai itaona anthu a Yoswawo, idachita zinthu mofulumira. Pamodzi ndi anthu ake idapita ku malo otsika oyang'anana ndi Araba, kuti ikamenyane ndi Aisraele kumeneko ngati kale lija. Iyo sinkadziŵa kuti aithira nkhondo cha kumbuyo kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pamene mfumu ya ku Ai anachiona, anafulumira iwo, nalawira mamawa, natuluka amuna a m'mudzi kuthirana ndi Israele, iye ndi anthu ake onse, poikidwiratu patsogolo pa chidikha; popeza sanadziwe kuti amlalira kukhonde kwa mudzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya Ai itaona ankhondo a Yoswa, inachita zinthu mofulumira. Inadzuka mmamawa ndipo inapita pamodzi ndi anthu ake ku malo otsika oyangʼanana ndi Araba kuti akachite nkhondo ndi Aisraeli. Koma iyo sinadziwe kuti ayithira nkhondo kudzera kumbuyo kwa mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pamene mfumu ya ku Ai anaciona, anafulumira iwo, nalawira mamawa, naturuka amuna a m'mudzi kuthirana ndi Israyeli, iye ndi anthu ace onse, poikidwiratu patsogolo pa cidikha; popeza sanadziwa kuti amlalira kukhonde kwa mudzi.