Joshua 8:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adauza Yoswa kuti, “Loza mkondo wako ku Ai. Mzindawu ndikukupatsa iwe.” Yoswa adachitadi monga adamuuzira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Tambasula nthungoyo ili m'dzanja lako iloze ku Ai, pakuti ndidzaupereka m'dzanja lako. Ndipo Yoswa anatambasula nthungoyo inali m'dzanja lake kuloza mudzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, “Loza mkondo uli mʼdzanja lako ku Ai pakuti ine ndipereka mʼdzanja lanu mzindawo.” Kotero Yoswa analoza mkondowo ku Ai.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Tambasula nthungo iri m'dzanja lako iloze ku Ai, pakuti ndidzaupereka m'dzanja lako. Ndipo Yoswa anatambasula nthungoyo inali m'dzanja lace kuloza mudzi.