Joshua 8:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzinda wa Ai ndi mfumu yake yomwe, muuchite zomwe mudachita Yeriko ndi mfumu yake. Koma katundu wamumzindamo ndi zoŵeta, musunge zikhale zanu. Muulalire mzindawo, ndipo muuthire nkhondo cha kumbuyo kwake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo uzimchitira Ai ndi mfumu yake monga umo unamchitira Yeriko ndi mfumu yake; koma zofunkha zake ndi ng'ombe zake mudzifunkhire nokha; udziikire anthu alalire kukhonde kwa mudzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mzinda wa Ai ndi mfumu yake muchite monga munachita ndi mzinda wa Yeriko ndi mfumu yake, koma katundu wa mumzindamo ndi zoweta mukazitenge ndi kuzisunga kuti zikhale zanu. Mukalalire mzinda wa Ai ndi kuwuthira nkhondo kuchokera kumbuyo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo uzimcitira Ai ndi mfumu yace monga umo unamcitira Yeriko ndi mfumu yace; koma zofunkha zace ndi ng'ombe zace mudzifunkhire nokha; udziikire anthu aja lire kukhonde kwa mudzi.