Joshua 8:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Ai aja atacheukira m'mbuyo adangoona utsi uli tolotolo! Malo oti iwowo athaŵireko panalibe, chifukwa choti Aisraele aja adaathaŵira kuthengoŵa adabwerera kudzalimbana nawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene amuna a ku Ai anacheuka, anapenya, ndipo taonani, utsi wa mudzi unakwera kumwamba; nasowa mphamvu iwo kuthawa chakuno kapena chauko; ndi anthu othawira kuchipululu anatembenukira owapirikitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Ai aja atangochewukira mʼmbuyo anaona utsi uli tolotolo. Koma mpata woti athawireko panalibe pakuti Aisraeli amene amathawira ku chipululu anabwerera nayamba kuwathamangitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene amuna a ku Ai anaceuka, anapenya, ndipo taonani, utsi wa mudzi unakwera kumwamba; nasowa mphamvu iwo kuthawa cakuno kapena cauko; ndi anthu othawira kucipululu anatembenukira owapitikitsa.