Joshua 8:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yoswa ndi anthu anali nawo aja, ataona kuti anzao aja alanda mzindawo, ndipo kuti utsi uli tolotolo, adatembenuka nayamba kupha anthu a ku Ai aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakupenya Yoswa ndi Israele yense kuti olalirawo adagwira mudzi, ndi kuti utsi wa mudzi unakwera, anabwerera, nawapha amuna a ku Ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoswa ndi Aisraeli onse ataona kuti obisalira aja alanda mzinda ndipo kuti utsi unali tolotolo, iwo anatembenuka ndi kuyamba kupha anthu a ku Ai.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakupenya Yoswa ndi Israyeli yense kuti olalirawo adagwira mudzi, ndi kuti utsi wa mudzi unakwera, anabwerera, nawapha amuna a ku Ai.