Joshua 8:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nawonso Aisraele amene anali mumzindamo adabwera kudzalimbana ndi anthu a ku Ai. Choncho onsewo anali atazingidwa ndi Aisraele, ndipo onsewo adaphedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
A kumudzinso anawatulukira; potero anakhala pakati pa Israele, ena mbali ina, ena mbali ina; ndipo anawakantha, mpaka sanatsale kapena kupulumuka wa iwo ndi mmodzi yense.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nawonso Aisraeli amene anali mu mzindamo anatuluka kudzalimbana ndi anthu a ku Ai. Choncho iwo anazingidwa mbali zonse ndi Aisraeli ndipo onse anaphedwa. Palibe amene anatsala wamoyo kapena wothawa
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
A kumudzinso anawaturukira; potero anakhala pakati pa Israyeli, ena mbali yina, ena mbali yina; ndipo anawakantha, mpaka sanatsala kapena kupulumuka wa iwo ndi mmodzi yense.