Joshua 8:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ya mzindawo adaipachika pa mtengo ndi kuisiya pompo mpaka madzulo. Madzulo ndi kachisisira, Yoswa adalamula kuti akatsitse mtembowo, ndipo atatero adautaya pansi ku chipata cha mzindawo. Pamwamba pa mtembowo adaunjikapo mulu wa miyala. Muluwo uli pomwepo mpaka lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya ku Ai, anampachika pamtengo mpaka madzulo; koma polowa dzuwa Yoswa analamulira kuti atsitse mtembo wake pamtengo; ndipo anauponya polowera pa chipata cha mudzi; naunjikako mulu waukulu wamiyala, mpaka lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anapachika pa mtengo mfumu ya Ai ndipo anayisiya mpaka madzulo. Pomwe dzuwa linalowa Yoswa analamula kuti akachotse mtembowo ndi kukawutaya ku chipata cha mzindawo. Pamwamba pa mtembowo anawunjikapo mulu waukulu wa miyala. Muluwo ulipobe mpaka lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya ku Ai, anampacika pamtengo mpaka madzulo; koma polowa dzuwa Yoswa analamulira kuti atsitse mtembo wace pamtengo; ndipo anauponya polowera pa cipata ca mudzi; nauniikako mulu waukuru wamiyala, mpaka lero lino.