Joshua 8:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adalimanga potsata malangizo amene Mose mtumiki wa Chauta adaapatsa Aisraele, ndi potsata mau a m'buku la malamulo a Mose onena kuti, “Guwa likhale la miyala yosasema ndi zipangizo zachitsulo.” Pa guwa limenelo adaperekapo nsembe zopsereza kwa Chauta, ndipo adaperekanso zopereka zamtendere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
monga Mose mtumiki wa Mulungu adalamulira ana a Israele, monga mulembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, guwa la nsembe la miyala yosasema, yoti palibe munthu anakwezapo chitsulo; ndipo anafukizirapo Yehova nsembe zopsereza, naphera nsembe zoyamika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Analimanga motsata zimene Mose mtumiki wa Yehova analamulira Aisraeli, ndiponso potsata zomwe zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Mose kuti guwa lansembe likhale la miyala yosasemedwa ndi chitsulo. Pa guwalo anapereka kwa Yehova nsembe yopsereza ndi nsembe yachiyanjano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
monga Mose mtumiki wa Mulungu adalamulira ana a Israyeli, monga mulembedwa m'buku la cilamulo ca Mose, guwa la nsembe la miyala yosasema, yoti palibe munthu anakwezapo citsulo; ndipo anafukizirapo Yehova nsembe zopsereza, naphera nsembe zoyamika.