Joshua 8:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele onse, pamodzi ndi atsogoleri ao, akuluakulu ao, aweruzi ao ndiponso alendo omwe amene anali pakati pao, adaimirira pa mbali ziŵiri za Bokosi lachipangano lija, ena uku ena uku, moyang'anana ndi ansembe Achilevi amene anali kunyamula Bokosilo. Theka lina la anthu lidaimirira kuyang'anana ndi phiri la Gerizimu, ndipo theka lina kuyang'anana ndi phiri la Ebala. Pachiyambi penipeni, Mose mtumiki wa Chauta adaaŵalamula iwowo kuti azichita zimenezi pofuna kulandira madalitso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aisraele onse, ndi akulu ao, ndi akapitao ao, ndi oweruza ao anaima chakuno ndi chauko cha likasa, pamaso pa ansembe Alevi, akusenza likasa la chipangano la Yehova, mbadwa ndi alendo omwe; ena a iwo pandunji pa phiri la Gerizimu, ndi ena pandunji pa phiri la Ebala; monga Mose, mtumiki wa Yehova, adalamulira poyamba paja kuti adalitse anthu a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli onse, akuluakulu awo, atsogoleri awo ndi oweruza awo, alendo pamodzi ndi mbadwa, anayimirira mbali zonse ziwiri za Bokosi la Chipangano la Yehova, ena uku ena uku moyangʼanana ndi ansembe a Chilevi. Theka la anthu linayima patsogolo pa phiri la Gerizimu ndipo theka lina patsogolo pa phiri la Ebala, monga momwe Mose mtumiki wa Yehova anawalamulira mʼmbuyomo pamene anawapatsa malangizo podalitsa Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Aisrayeli onse, ndi akuru ao, ndi akapitao ao, ndi oweruza ao anaima cakuno ndi cauko ca likasa, pamaso pa ansembe Alevi, akusenza likasa la cipangano la Yehova, mbadwa ndi alendo omwe; ena a iwo pandunji pa phiri la Gerizimu, ndi ena pandunji pa phiri la Ebala; monga Mose, mtumiki wa Yehova, adalamulira poyamba pala kuti adalitse anthu a Israyeli,