Joshua 9:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafumu onse okhala kuzambwe kwa Yordani adamva zimenezi. Onse okhala ku mapiri, m'zigwa ndiponso m'mbali mwa Nyanja Yaikulu cha kumpoto kwa Lebanoni, nawonso adamva. Ameneŵa ndiwo mafumu a Ahiti, Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakumva ichi mafumu onse a tsidya ilo la Yordani, kumapiri ndi kuchidikha, ndi ku madooko onse a Nyanja Yaikulu, pandunji pa Lebanoni: Ahiti ndi Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafumu onse okhala kumadzulo kwa Yorodani atamva zimenezi pamodzi ndi mafumu okhala ku mayiko a ku mapiri, mu zigwa, mʼmbali mwa Nyanja yayikulu mpaka ku Lebanoni (mafumu a Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi),
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yoswa anyengedwa ndi Agibeoni napangana nao. Ndipo kunali, pakumva ici mafumu onse a tsidya ilo la Yordano, kumapiri ndi kucidikha, ndi ku madoko onse a nyanja yaikuru, pandunji pa Lebano: Ahiti ndi Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;