Joshua 9:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patangopita masiku atatu atachita chipanganocho, Aisraele adaŵazindikira anthuwo kuti ngochokera pafupi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, atatha kupangana nao masiku atatu, anamva kuti ndiwo anansi ao, ndi kuti kwao ndi pakati pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patatha masiku atatu atachita mgwirizano wa mtendere ndi Agibiyoni, Aisraeli anamva kuti anali anansi awo, anthu amene amakhala nawo pafupi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, atatha kupangana nao masiku atatu, anamva kuti ndiwo anansi ao, ndi kuti kwao ndi pakati pao,