Joshua 9:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komatu Aisraele sadathe kuŵapha anthuwo, poti paja atsogoleri ao anali atalonjeza m'dzina la Chauta, Mulungu wa Israele, za anthu ameneŵa; apo Aisraele ena adayamba kudandaula kwa atsogoleri za zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele sanawakanthe, pakuti akalonga a msonkhano adawalumbirira kwa Yehova, Mulungu wa Israele. Ndipo msonkhano wonse unadandaula pa akalonga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Aisraeli sanawaphe anthuwo chifukwa atsogoleri awo anali atalonjeza mʼdzina la Yehova Mulungu wa Israeli za Agibiyoniwo. Koma anthu onse anatsutsana ndi atsogoleriwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli sanawakantha, pakuti akalonga a msonkhano adawalumbirira kwa Yehova, Mulungu wa Israyeli. Ndipo msonkhano wonse unadandaula pa akalonga,