Joshua 9:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo iwo adayankha kuti, “Mbuyathu, ife tidachita zimenezi chifukwa choti tidamva kuti Chauta, Mulungu wanu, adalamula mtumiki wake Mose kuti adzakupatseni dziko lonseli, ndipo kuti mudzaphe anthu onse kulikonse kumene mukaŵapeze. Motero tidachita zimenezi poti tidakuwopani kwambiri ndipo tidafuna kupulumutsa moyo wathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wake Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m'dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinachita chinthuchi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anayankha Yoswa kuti, “Ife akapolo anufe tinachita zimenezi chifukwa tinamva bwino lomwe kuti Yehova Mulungu wanu analamula Mose mtumiki wake kuti adzakupatsani dziko lonseli ndi kuti anthu onse okhalamo adzaphedwe. Tsono ife tinachita mantha aakulu ndipo tinachita zimenezi pofuna kupulumutsa miyoyo yathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wace Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m'dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinacita cinthuci.